Aefeso 1:11 - Buku Lopatulika Mwa Iye tinayesedwa akeake olandira cholowa, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake, |
Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.
Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana.
amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe!
Pakuti ndani waima mu upo wa Yehova, kuti aone namve mau ake? Ndani wazindikira mau anga, nawamva?
wamkulu mu upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;
inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri.
Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.
ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;
Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa.
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.
ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;
ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.
pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,
Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.
ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,
Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,
Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,
monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:
Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.
ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;
podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.
Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?
kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.