Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.
2 Yohane 1:8 - Buku Lopatulika Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma yesetsani kuti mukalandire mphotho yathunthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse. |
Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.
Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.
Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.
Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.
Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.
Koma tadzikumbutsani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa;
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;