2 Yohane 1:11 - Buku Lopatulika Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti wopatsa munthu wotere moni, akuvomereza zochita zake zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa. |
Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.
koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.
Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;