Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu.
2 Yohane 1:10 - Buku Lopatulika Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wina aliyense akadza kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamlandire m'nyumba mwanu. Musampatse ndi moni womwe, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. |
Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu.
Nati iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano;
Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.
Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:
koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.
Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata iyi, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.
Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo.