Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
2 Timoteyo 4:4 - Buku Lopatulika ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe. |
Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;
Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.
Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;
kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;
koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;
Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama;
Ichi uchidziwa, kuti onse a mu Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Figelo ndi Heremogene.
osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.
Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.