Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.
2 Timoteyo 4:2 - Buku Lopatulika lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa. |
Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.
Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;
Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.
Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.
Tsiku la Sabata tinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.
Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.
amene ndinakhala mtumiki wake, monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakuchitira inu, wakukwaniritsa mau a Mulungu,
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.
wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,
Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m'chikhulupiriro,
Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule.
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.