2 Timoteyo 3:7 - Buku Lopatulika ophunzira nthawi zonse, koma sangathe konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa amangomvera za aliyense, ndipo sangathe konse kudziŵa choona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi. |
Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.
Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.
wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,
Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otivuta powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.