Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
2 Samueli 6:15 - Buku Lopatulika Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho iye pamodzi ndi Aisraele onse adabwera ndi Bokosi lachipangano akufuula ndi kuliza mbetete. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga. |
Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.
Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.
Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera.
Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.