2 Samueli 3:33 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Polira maliro a Abinere mfumu Davide ankati, “Abinere nkufa motere, monga m'mene chimafera chitsiru? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri: “Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru. |
Manja anu sanamangidwe, mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo; monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu. Ndipo anthu onse anamliranso.
Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.
Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.
Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana aakazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.