Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?
2 Samueli 23:39 - Buku Lopatulika Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uriya Muhiti uja. Onse pamodzi anali anthu 37. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi Uriya Mhiti. Onse pamodzi analipo 37. |
Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?
Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.
chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.
Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.