Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe.
pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efayi wa ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao.