Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.
2 Samueli 22:50 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Chifukwa cha zimenezi ndidzakuyamikani Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu. |
Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.
Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.