Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.
2 Samueli 22:49 - Buku Lopatulika Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinu amene mudandipulumutsa kwa adani anga. Mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza. |
Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.
Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israele, ndi kuti anakulitsa ufumu wake chifukwa cha anthu ake Israele.
Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa.
Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.
Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa.
Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.