2 Samueli 22:42 - Buku Lopatulika Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakuwa, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woŵapulumutsa. Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe. |
Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.
Tsiku limenelo munthu adzayang'ana kwa Mlengi wake, ndipo maso ake adzalemekeza Woyera wa Israele.
Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.
Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.
Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.
Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.