Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
2 Samueli 22:41 - Buku Lopatulika Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo, kuti ndiwalikhe akudana ndi ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo, kuti ndiwalikhe akudana ndi ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mudapirikitsa adani anga kuti andithaŵe, amene ankadana nane ndidaŵaononga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa; ndipo ndinawononga adani anga. |
Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.
Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.
Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.
Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana aamuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.