2 Samueli 22:37 - Buku Lopatulika Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga, ndi mapazi anga sanaterereke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga, ndi mapazi anga sanaterereke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwalimbitsa miyendo yanga kuti ndiyende bwino, choncho mapazi anga sadaterereke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino, kuti mapazi anga asaterereke. |
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.