2 Samueli 22:35 - Buku Lopatulika Iye aphunzitsa manja anga nkhondo; kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo; kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo. |
Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao:
Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.
ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja.
Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.