Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.
2 Samueli 22:29 - Buku Lopatulika Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu Inu Chauta, ndinu nyale yanga, Inu Mulungu, mumandiwunikira mu mdima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, ndinu nyale yanga; Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika. |
Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.
Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.
Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.
Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.
Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.
Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.