Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.
2 Samueli 21:21 - Buku Lopatulika Ndipo pakutonza Israele iyeyu, Yonatani mwana a Simea mbale wa Davide anamupha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakutonza Israele iyeyu, Yonatani mwana a Simea mbale wa Davide anamupha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene iye ankanyoza Aisraele, Yonatani mwana wa Simea, mbale wa Davide, adamupha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha. |
Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.
Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.
Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.
Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?
ndi Yese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliyabu, ndi Abinadabu wachiwiri, ndi Simea wachitatu,
Ndipo Yonatani atate wake wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;
Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.
Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa.
Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.