2 Samueli 21:17 - Buku Lopatulika
Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.
Onani mutuwo

Koma Abisai, mwana wa Zeruya, adabwera kudzathandiza Davide, nalimbana ndi Mfilistiyo mpaka kumupha. Tsono anthu a Davide adamlonjeza molumbira Davideyo kuti, “Tsopano inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuwopa kuti mungaphedwe. Inu ndinu amene Aisraele onse amagonerapo.”
Onani mutuwo
Koma Abisai mwana wa Zeruya anabwera kudzapulumutsa Davide. Iye anamukantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti, “Inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuti nyale ya Israeli isadzazimitsidwe.”
Onani mutuwo