Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 21:15 - Buku Lopatulika

Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nthaŵi ina Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele. Davide adapita ndi ankhondo ake, nakamenyana nawo nkhondo Afilistiwo, ndipo iyeyo adatopa kwambiri.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nthawi inanso panali nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraeli, Davide anapita ndi ankhondo ake kukamenyana ndi Afilisti ndipo iye anatopa kwambiri.

Onani mutuwo



2 Samueli 21:15
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.


Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja.


Ndipo Afilisti anakweranso kachiwiri, natanda m'chigwa cha Refaimu.


Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezere.


Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.


Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezere ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Sipai wa ana a chimphona; ndipo anawagonjetsa.


Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.


Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.


Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.


tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;