Ndipo Yowabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupirikitsa Aisraele; pakuti Yowabu analetsa anthuwo.
2 Samueli 20:22 - Buku Lopatulika Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka pamudzipo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka mkaziyo mwa nzeru zake adapita kwa anthu, naŵasimbira nkhaniyi. Choncho anthuwo adadula mutu wa Sheba, mwana wa Bikiri, namponyera Yowabu. Pamenepo Yowabu adaliza lipenga, ndipo ankhondo ake adachoka kumzindako, aliyense kupita kwao, ndipo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu. |
Ndipo Yowabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupirikitsa Aisraele; pakuti Yowabu analetsa anthuwo.
Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.
Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso.
Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.
Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mzindamo anafuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yowabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndilankhule nanu.
Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.