Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.
2 Samueli 20:14 - Buku Lopatulika Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sheba adapita ndithu kubzola mafuko onse a Aisraele mpaka kukafika ku Abele wa ku Betemaki. Abikiri onse adasonkhana, naloŵa naye mumzindamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Seba anadutsa mafuko onse a Israeli mpaka ku Abeli ndi Beti-Maaka ndiponso chigawo chonse cha Abeli, amene anasonkhana pamodzi ndi kumutsata iye. |
Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.
Ndipo anadza nammangira misasa mu Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mzindawo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse.
Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumizinda ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali.
Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.
Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi mizinda ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi mizinda yonse ya chuma ya Nafutali.
Ndipo atachokapo anamuka ku Beere, ndicho chitsime chimene Yehova anachinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.