Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mzinda wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.
2 Samueli 19:38 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mfumu idayankha kuti, “Kimuhamu ndiwoloka naye limodzi, ndipo ndidzamchitira chilichonse chimene chikukomereni inu. Ndipo zonse zimene mufuna kuti ndikuchitireni, ndidzakuchitirani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inati, “Kimuhamu adzawoloka ndi ine, ndipo ndidzamuchitira iye chilichonse chimene chidzakondweretsa iwe. Ndipo chilichonse chimene udzandipempha ine ndidzakuchitira.” |
Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mzinda wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.
Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.
Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.
ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,