Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.
2 Samueli 19:21 - Buku Lopatulika Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pompo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa kuti, “Kodi Simeiyu ndiye saphedwa chifukwa chotukwana wodzozedwa wa Chauta?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati, “Kodi Simei saphedwa chifukwa cha ichi? Iye anatukwana wodzozedwa wa Yehova.” |
Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake.
Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,
Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?