2 Samueli 18:33 - Buku Lopatulika Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo mfumu idagwidwa ndi chisoni chachikulu, nikwera ku chipinda cham'mwamba pa chipata kukalira. Tsono popita inkati, “Iwe mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu. Kalanga ine, achikhala ndidaafa ndine m'malo mwako! Iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inanthunthumira. Inapita ku chipinda cha mmwamba cha pa chipata kukalira. Pamene imapita, inkati: “Iwe mwana wanga Abisalomu! Mwana wanga! Mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine mʼmalo mwako! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” |
Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.
Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana.
Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m'buku lanu limene munalembera,
Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;
Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.