Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, nanka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu.
2 Samueli 17:15 - Buku Lopatulika Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Husai adauza Zadoki ndi Abiyatara, ansembe aja, kuti, “Zimene Ahitofele adaalangiza Abisalomu ndi atsogoleri a Aisraele ndi izi, izi. Koma ineyo ndaŵalangiza izi, izi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Husai anawuza ansembe Zadoki ndi Abiatara kuti, “Ahitofele analangiza Abisalomu ndi akuluakulu a Israeli zakuti, koma ine ndawalangiza kuchita zakutizakuti. |
Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, nanka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu.
ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.