Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
2 Samueli 16:20 - Buku Lopatulika Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abisalomu adafunsa Ahitofele kuti, “Iwe ukuganiza bwanji pamenepa? Tsopano tichite chiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?” |
Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu.
Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi aang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisraele onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.
Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.
Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?
Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.
Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;