Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?
2 Samueli 16:18 - Buku Lopatulika Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Husai adayankha Abisalomu kuti, “Iyai, munthu amene wasankhidwa ndi Chauta ndiponso ndi anthu aŵa, kudzanso amuna onse a Aisraele, ndiye ndidzakhale mtumiki wake, ndipo ndidzakhala pambuyo pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse. |
Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?
Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu.
Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.