Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
2 Samueli 16:15 - Buku Lopatulika Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse aamuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse amuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abisalomu ndi Aisraele onse amene anali naye, kudzanso Ahitofele, adaaloŵa mu Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye. |
Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai Mwariki anadzakomana naye ali ndi malaya ake ong'ambika, ndi dothi pamutu pake.
Chomwecho Husai bwenzi la Davide anadza m'mzindamo; ndipo Abisalomu anafika ku Yerusalemu.
Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko.