2 Samueli 14:33 - Buku Lopatulika Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yowabu adapita kwa mfumu, nakakambira mfumuyo zimenezo. Tsono mfumu idaitana Abisalomu. Iye adabwera kwa mfumu, nadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Ndipo mfumuyo idamlandira bwino pakumumpsompsona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anayiwuza zimenezi. Ndipo mfumu inamuyitanitsa Abisalomu, ndipo analowa nawerama kugunditsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Tsono mfumu inapsompsona Abisalomu. |
Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.
Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu aliyense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lake, namgwira, nampsompsona.
Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.
Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu.
Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.