Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
2 Samueli 13:33 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi chinthuchi, ndi kuganiza kuti ana aamuna onse a mfumu afa; pakuti Aminoni yekha wafa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi chinthuchi, ndi kuganiza kuti ana amuna onse a mfumu afa; pakuti Aminoni yekha wafa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake tsono mbuyanga mfumu, musavutike ndi maganizo oti ana anu onse aamuna aphedwa. Aminoni yekha ndiye waphedwa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.” |
Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.