Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mzinda wa pamadzi.
2 Samueli 12:28 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mzindawo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mzindawo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mudziwo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mudziwo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono inu musonkhanitse ankhondo onse otsala, ndipo bwerani mudzauzinge ndi zithando mzindawo ndi kuulanda, kuwopa kuti ine ndikalanda mzindawo, ungamatchedwe dzina langa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.” |
Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mzinda wa pamadzi.
Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.