Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
2 Samueli 12:27 - Buku Lopatulika Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mzinda wa pamadzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mudzi wa pamadzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatuma amithenga kwa Davide kukamuuza kuti, “Ndauthira nkhondo mzinda wa Raba, ndipo ndalanda nkhokwe yake ya madzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi. |
Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mzindawo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mzindawo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa.
Uiike njira yodzera lupanga kunka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.
(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).