Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
2 Samueli 12:26 - Buku Lopatulika Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mzinda wachifumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wachifumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imeneyo Yowabu ndi ankhondo a Aisraele ankathira nkhondo Raba, likulu la Aamoni, ndipo anali pafupi kuulanda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu. |
Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.
natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mzinda wa pamadzi.
Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,
Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).