Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
2 Samueli 12:21 - Buku Lopatulika Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono atumiki ake aja adamufunsa kuti, “Tatifotokozerani, kodi zimene mwachitazi nzotani? Pamene mwana uja anali moyo, inu munkakana kudya. Koma pamene adamwalira, inu mudadzuka, nkuyamba kudya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!” |
Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandichitira chifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.
Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.