Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:
2 Samueli 12:17 - Buku Lopatulika Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akuluakulu a ku nyumba ya mfumu adadzaima pambali pake kuti amuutse. Koma iye adakana kuuka, ndipo sadadye nawo chakudya anthuwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo. |
Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:
Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga?
Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira.
Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama.