2 Samueli 1:27 - Buku Lopatulika Ha! Amphamvuwo anagwa, ndi zida za nkhondo zinaonongeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ha! Amphamvuwo anagwa, ndi zida za nkhondo zinaonengeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ha! Kani amphamvu agwa motere, zida zao zankhondo nkuwonongeka!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Taonani amphamvu agwa! Zida zankhondo zawonongeka!” |
Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!
Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.
Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.
Achokera m'dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.