Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 1:15 - Buku Lopatulika

Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pomwepo Davide adaitana mmodzi mwa ankhondo ake, namuuza kuti, “Mtenge ameneyu, ukamuphe.” Wankhondoyo adamkanthadi naafa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa.

Onani mutuwo



2 Samueli 1:15
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Solomoni anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.


Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m'nyumba yakeyake kuchipululu.


Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.


Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.


Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.


Nati kwa Yetere mwana wake woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.