Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Mbiri 4:3 - Buku Lopatulika

Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

M'munsi mwa milomomu adaazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo zithunzi zangʼombe zazimuna mozungulira, zithunzi khumi pa theka la mita. Ngʼombezo zimajambulidwa mʼmizere iwiri ndipo anazipangira kumodzi ndi mbiyayo.

Onani mutuwo



2 Mbiri 4:3
8 Mawu Ofanana  

Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.


Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi mbuyo zao zinayang'anana.


Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.


Ndipo aliyense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yachiwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yachitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yachinai ndiyo nkhope ya chiombankhanga.


Ndipo muzizungulira mzinda inu nonse ankhondo, kuuzungulira mzinda kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.


Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang'ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka.