Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Mbiri 1:3 - Buku Lopatulika

Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Solomoni pamodzi ndi anthu onse amene adasonkhana nawo, adapita ku kachisi wa ku Gibiyoni. Paja chihema chamsonkhano cha Mulungu chimene Mose, mtumiki wa Chauta, adaamanga ku chipululu chinali kumeneko.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la anthu anapita ku malo ofunika kwambiri pachipembedzo ku Gibiyoni. Tenti ya msonkhano ya Mulungu inali kumeneko, imene Mose mtumiki wa Yehova anayipanga mʼchipululu muja.

Onani mutuwo



2 Mbiri 1:3
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.


ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku chihema cha Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;


Pakuti chihema cha Yehova amene Mose anapanga m'chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi.


Momwemo Solomoni anadza ku Yerusalemu kuchokera ku msanje uli ku Gibiyoni, ku khomo la chihema chokomanako; ndipo anachita ufumu pa Israele.


Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri.


Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako.


Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.


Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'chihema chokomanako Iye, nati,


Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova.


Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,