Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo;
2 Mafumu 9:9 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chautayo adzasandutsa banja la Ahabu kuti lifanane ndi banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso la Baasa mwana wa Ahiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. |
Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo;
ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.
Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.