Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.
2 Mafumu 8:2 - Buku Lopatulika Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero maiyo adanyamuka, ndipo adachitadi monga momwe munthu wa Mulungu uja adaanenera. Adapita pamodzi ndi a pabanja pake, nakakhala nawo ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri. |
Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.
Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati.