2 Mafumu 7:6 - Buku Lopatulika
Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.
Onani mutuwo
Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.
Onani mutuwo
Chauta anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lankhondo pakati pa ankhondo a Asiriya. Ndiye iwowo adayamba kuuzana kuti, “Tamvani phokosolo, mfumu ya ku Israele yalemba mafumu a Ahiti ndi a Aejipito kuti adzatithire nkhondo!”
Onani mutuwo
pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!”
Onani mutuwo