2 Mafumu 4:3 - Buku Lopatulika Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Elisayo adamuuza kuti, “Pitani, kabwerekeni mitsuko yambirimbiri kwa anzanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Elisa anati, “Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa. |
Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.
Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako aamuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.
Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukuchotsa kudziko la Ejipito; yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.
Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.