Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
2 Mafumu 4:2 - Buku Lopatulika Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Elisa adafunsa maiyo kuti, “Nanga mukuti ineyo nditani? Tanenani, muli ndi chiyani m'nyumba mwanu?” Maiyo adayankha kuti, “Mdzakazi wanune ndilibe nkanthu komwe m'nyumba, koma kambiya ka mafuta basi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.” |
Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha chimene ndikuchitire ndisanachotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.
Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono.
Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.
monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?