Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.
2 Mafumu 3:8 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku chipululu cha Edomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku chipululu cha Edomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yehosafatiyo adafunsa kuti, “Kodi tidzere njira iti popita kunkhondoko?” Yoramu adayankha kuti, “Tidzere ku chipululu cha Edomu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?” Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.” |
Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.
Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.
Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.