2 Mafumu 15:3 - Buku Lopatulika Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Azariya adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyo anachita zabwino pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake. |
Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.
Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya.
Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.