Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.
2 Mafumu 11:3 - Buku Lopatulika Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwanayo adakhala ndi mlezi wake zaka zisanu ndi chimodzi akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo. |
Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.
Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi chimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.
Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anam'bisa miyezi itatu.
Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.
Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.