musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.
2 Mafumu 10:4 - Buku Lopatulika Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthuwo adachita mantha kwambiri, ndipo adati, “Ha! Mafumu aŵiri aja sadathe kulimbana naye Yehu, nanga ife ndiye tingathe bwanji?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anthuwo anachita mantha kwambiri ndipo anati, “Taonani, mafumu awiri sanathe kulimbana naye, nanga ife tingathe bwanji?” |
musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.
Yehu anakoka uta wake ndi mphamvu zonse, nalasa Yoramu pachikota, nupyoza muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m'galeta wake.
Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.
Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? Ndiziponde ndizitenthe pamodzi.
Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?
Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.
Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sayamba wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri?